• National Economic Empowerment Fund (NEEF), Malawi


post-image
Mtsogoleri wa gulu lotchedwa Mtendere irrigation scheme, a January Chiwere ati ngongole ya ulimi wa mthilira yomwe anatenga ku bungwe la National Economic Empowerment Fund (NEEF), yawathandizira kuthetsa njala pakhomo lawo.

Gulu la Mtendere irrigation scheme lomwe lili ndi mamembala 52 kuphatikiza amayi, abambo ndi achinyamata lili m'mudzi mwa Dzimphutsi mfumu yayikulu Maseya m'boma la Chikwawa.

A Chiwere ati gulu limeneli linatenga ngongole yokwana 17 Miliyoni Kwacha, kuti alime chimanga pa ma ekala okwana 62. Ndipo iwo ati pawokha adatenga matumba awiri a feteleza ndikulima ekala imodzi.

A Chiwere anafotokozaso kuti chaka chino akolola zochuluka kuposa zaka za m’mbuyomu ndipo ayamikira bungwe la NEEF chifukwa cha thandizoli. "Ndikuyamika bungwe la NEEF chifukwa landithandiza kupeza zokolola zochuluka kusiyana ndi zaka zam'mbuyomu pomwe ndimapeza matumba osakwana khumi. Chimanga chomwe ndapeza chitha kupitilira matumba makumi awiri olemela makilogalamu makumi asanu (50), ndipo izi zipangitsa kuti ndibwenze ngongoleyi mosavuta komanso kutsala ndi chakudya chokwanira," anatero a Chiwere.

Pamapeto pake iwo apempha bungwe la NEEF kuti lipitililebe kupereka ngongoleyi kwa alimi kuti akhale ndi chakudya chokwanira pakhomo pawo.
Malingana ndi a Chiwere, ngongole ya NEEF ndi njira imodzi yolimbana ndi njala ndi kusintha miyoyo maka kwa anthu omwe ali ndi chidwi pa ulimi.


#NEEF
#UlimiwaMthilira