• National Economic Empowerment Fund (NEEF), Malawi

SATISFIED CLIENTS


Uploaded Image

Agness Gera Farmer, Agro-trader, and Mobile money agent

"In 2021 despite my ongoing work, I recognized the need for financial support and NEEF came to my rescue once more. With the loan, I ventured into cattle farming, supplying milk across Liwonde and creating job opportunities for others."
Uploaded Image

Bwanali Salanje Dedza Resident

"All of these problems are now history thanks to the NEEF loan because I am now able to provide for my familyโ€™s needs, pay for my childrenโ€™s education, and my business has grown."
Uploaded Image

Boyson Kabvina Phiri Farmer

"I have managed to produce 100 bales of tobacco ready to be transported to auction floors for selling and am optimistic that I will manage to pay back the loan in time"
Uploaded Image

๐‘๐ข๐ฌ๐ข๐ง๐  ๐…๐ซ๐จ๐ฆ ๐€๐ฌ๐ก๐ž๐ฌ; ๐‚๐ก๐š๐ญ๐ฌ๐ž๐ค๐š'๐ฌ ๐๐ฎ๐ฌ๐ข๐ง๐ž๐ฌ๐ฌ ๐‘๐ž๐ฏ๐ข๐ฏ๐š๐ฅ ๐ฐ๐ข๐ญ๐ก ๐๐„๐„๐… ๐‹๐จ๐š๐ง๐ฌ

"Women financial empowerment is one of the key milestones that National Economic Empowerment Fund (NEEF) limited strives to achieve. Ensuring that women become key actors in Agriculture entrepreneurship and any other form of business is essential for Malawiโ€™s economic growth."
Uploaded Image

CHIPINI MEN- OPINDULA NDI NGONGOLE YA NEEF

"Chipini Men ochokela m'mudzi mwa mfumu yaikulu Mwenelufita, T/A Mwaulambya Ku Chitipa Central kulandira matumba okwana 32 a UREA kupindula ndi ndondomeko ya ngongole ya zipangizo za ulimi."
Uploaded Image

Mbununu Men's Club

"Gulu la Mbununu Mens Club kuchokela m'mudzi mwa Chilima T/A Chimutu ku Lilongwe poyambilira anatenga ngongole ya MK5,000,000 ya bizinezi ndipo pano anapempha ngongole ya MK30,000,000 kudzera mu ndondomeko ya ngongole ya zipangizo za ulimi. Gululi lalandila matumba 258 a feteleza omwe 129 ndi a NPK komaso 129 ndi matumba a UREA."
Uploaded Image

Pemphero Tchauya Men

"Pemphero Tchauya Men ya m'mudzi mwa Kuchisambo T/A Chilikumwendo kwa Lobi Ku Dedza anapempha ngongole yokwana 9 Million Kwacha kudzera mu ndondomeko ya ngongole ya zipangizo za ulimi ndipo alandira matumba a feteleza okwana 75 a UREA."
Uploaded Image

Chitatata Women's

"Chitatata Women group ya m'mudzi mwa mpundu, mfumu yaikulu Matepo T/A Timbili ku Nkhatabay- Northwest Constituency alandira matumba okwana 19 a feteleza pomwe anafunsa ngongole ya zipangizo za ulimi yomwe bungwe la NEEF likupeleka."
Uploaded Image

Chipulikano Women's

"Chipulikano Women's Club ya m'mudzi mwa Zuwayumo kwa T/A M'Mbwelwa alandira matumba a feteleza okwana 20 Bags a NPK kudzera mu ndondomeko ya ngongole ya zipangizo za ulimi."
Uploaded Image

Mpoto Club

"Mpoto Club ya m'mudzi mwa Chihepa kwa T/A Mabilabo yapindura nawoso ndi ndondomeko ya ngongole ya zipangizo za ulimi pomwe alandira matumba a feteleza okwana 21 a NPK kudzera mu ngongole yomwe anapempha yokwana 7 million kwacha."
Uploaded Image

Sekelelani Men

"Abambo a gulu la Sekelelani 1 a m'mudzi mwa Chowezga T/A Khosolo alandila matumba okwana 16 a NPK kudzera mu ngongole ya zipangizo za ulimi yomwe anapempha yokwana 15 Million kwacha."
Uploaded Image

Chipembere Youth

"Gulu la Chipembere Youth lomwe limachokera m'mudzi mwa Malimba T/A Chimwendo kwa Lobi, Dedza linapempha ngongole yokwana 10 million kwacha ndipo alandila matumba okwana 83 kudzera mu ndondomeko ya ngongole ya zipangizo za ulimi."
Uploaded Image

M'boloma Men

"M'dalitso wa laMulungu sunawadutse abambo a gulu la M'boloma omwe amachokela m'mudzi mwa Lundu T/A Chapananga pamene alandira matumba okwana 15 a Urea kudzera mu ndondomeko ya ngongole ya zipangizo za ulimi."
Uploaded Image

Thukutalathu Women

"Nawo azimayi a Thukutalathu-2 omwe amachokela m'mudzi mwa mfumu yaikulu Nyangu T/A Makhwira Ku East Bank Ku Chikwawa akusimba lokoma atalandira matumba awo okwana 36 a Urea pomwe zatheka kudzera mu ndondomeko ya ngongole ya zipangizo za ulimi."
Uploaded Image

Malosa Men

"Gulu la abambo a Malosa omwe amachokera m'mudzi mwa Kapichira T/A Kapelula ku Kasungu anapempha 15 million kwacha kudzera mu ndondomeko ya ngongole ya zipangizo za ulimi. Iwo alandira matumba okwana 50 a feteleza wa UREA."
Uploaded Image

Mdalitso Club

"Mdalitso club yochokela m'mudzi mwa Makhosana kwa T/A Khosolo Ku Mzimba alandira matumba okwana 34 a UREA pamene anapempha ndalama zokwana 13 Million kwacha kudzera mu ndondomeko ya ngongole ya zipangizo za ulimi."
Uploaded Image

Kanono Club

"Kanono Club ya m'mudzi mwa Bisa Phiri kwa T/A Khosolo Ku Mzimba anapempha ngongole yokwana 13 million kwacha Ku bungwe la NEEF. Gululi lalandira matumba 55 a UREA."
Uploaded Image

Senior Chief Dambe

"Senior Chief Dambe kuchokera Ku Mchinji East constituency boma la Mchinji alandira Matumba 30 a UREA. Iwo anapempha ngongole ya NEEF kudzera mu ndondomeko ya ngongole ya zipangizo za ulimi (Farm Input Loan)."
Uploaded Image

Chigwirizano Women

"Amayi a gulu la Chigwilizano omwe amachokera m'mudzi mwa Mwalukira kwa T/A Nthondo ku north east constituency m'boma la Ntchisi alandira matumba okwana makumi awiri ndi mphambu zinayi (24) kudzera mu ndondomeko ya zipangizo za ulimi kuchokera ku bungwe la NEEF."
Uploaded Image

Mwambo Ogawa Ngongole ya Zipangizo za Ulimi kwa Kalolo

"Olemekeza a Horace Chipuwa omwe ndi phungu wa nyumba ya malamulo mothandizana ndi a T/A Kalolo kupeleka feteleza kwa alimi ochokela mwa amfumu a Kalolo mโ€™boma la Lilongwe, komwe kwagawidwa matumba 800 a feteleza wa mu ndondomeko ya ngongole ya zipangizo za ulimi zomwe bungwe la NEEF likupeleka."