Bungwe lobwereketsa ndalama la National Economic Empowerment Fund (NEEF) latsimikiza kudzipereka pakukweza chitukuko cha ulimi ku Malawi kudzera mu mapulani atsopano azachuma omwe alimbikitsa ulimi wa chaka chonse.
Izi zalengezedwa pamsonkhano waukulu womwe unakonzedwa ndi Unduna wa zamalimidwe ku Hotela ya Lilongwe Crossroads, komwe alangizi a za ulimi omwe amagwira ntchito yothandiza alimi adasonkhana kuti akambirane zovuta, apeze mayankho, komanso agawane malingaliro pa momwe angapititsire patsogolo gawo lokweza chuma chadziko lino motsatira masomphenya a chaka cha 2063 a dziko la Malawi.
Potsekulira mwambowu, Nduna ya zamalimidwe, Olemekezeka Sam Kawale, adalongosola kuti msonkhanowu ukhala mwayi wogawana ndondomeko zatsopano za ulimi zomwe unduna wake ukukwaniritsa.
βUnduna wathu wayambitsa njira zothandiza alimi kuyamba ulimi wothirira kuti dziko lizikhala ndi chakudya chokwanira nthawi zonse. Kuphatikiza apo, undunawu ukugwira ntchito ndi nthambi zina za boma monga bungwe la NEEF ndi ma bungwe ena omwe achilimika kwambiri pa nkhani ya ulimi mdziko muno,β Kawale kufotokoza.
Mkulu wa bungwe la National Economic Empowerment Fund Limited (NEEF), Humphrey Mdyetseni, anati pofuna kuwonetsetsa kuti ntchito za bungwe la NEEF zikuchitika mwachangu komanso mwadongosolo, awonetsetsa kuti ku ma ofesi a Extension Planning Areas (EPAs) kukhazikitsidwe alangizi a NEEF, Agricultural Loan Officers omwe adziwona za ngongole za ulimi mothandizana ndi mlangizi wa zamalimidwe.
"Izi zikudza chifukwa ndondomeko yathu ndiyakuti, ngongole ya mthirira ya ulendo uno tiyamba mwezi wa April mpaka September ndi cholinga chakuti ndondomekoyi ithandize alimi 400,000, kupereka chithandizo cha ndalama pa ma ekala oposera 50,000, komanso kupereka zipangizo zofunika mu ulimi monga matumba 200,000 a feteleza komanso 500 metric tons ya mbewu, ndi mankhwala," adatero Mdyetseni.
Bungwe la NEEF likugwira ntchito yotamandika kwambiri posintha makhalidwe a ulimi ku Malawi, kuonetsetsa kuti alimi akulandira zipangizo zofunika kuti achite ulimi wokhazikika komanso wopindulitsa.