
Magulu komanso anthu osiyanasiyana kuchokera m’boma la Dedza akusimba lokoma pomwe ngongole yomwe adatenga ku bungwe la NEEF apindula nayo mopsola muyeso.
Polankhula ndi Kondwani Kawerenga ochokera kwa Senior Chief Kafere M’boma la Dedza, yemwe ndi membala wagulu la Bridge Mseche ndipo adatenga ndalama kubungwe la National Economic Empowerment Fund Limited (NEEF) ulendo uwiri, wanenetsa kuti ngongole yabungweli ikupereka thandizo lopezekeratu m’mabanja awo.
“Ineyo ndinene zowona ngongoleyi yandibweretsera thandizo lalikulu pa nyumba panga. Ndidamanga nyumba yomwe muli wa rent mphunzitsi,ndidagula chigayo chakuswa mtedza, ndipo banja langa likukhala mosangalala kwambiri kusiyanitsa ndi nthawi imene ndinali ndisanatenge ngongoleyi,” atero bambo Kawerenga.
Ndipo a Daless Katsika yemwe ndi msungi chuma wa Magomero Dairy Farmers Cooperative ndipo amapanga bizinezi ya golosale, adatenga ndalama yokwana 1 miliyoni wanenetsa kuti ngakhale kuti ng’ombe zake zimatulutsa mkaka wambiri ndipo pa mwezi amatenga ndalama zochulukirapo iye adaona cha zeru kuti akhaleso ndi bizinezi ina yomwe izimudyetsa tsikulirilonse, kotero kuti iye wakwanitsa kugula malo ndi zinthu zina zambiri.
“kuti tidzidalira ndalama yapamwezi ndekuti sitidya mchifukwa chake nditatenga ndalamayo ndidayiponya ku bizinezi yangayi, ndipo ndikupeza phindu lochuluka kuchokera ku bizinezi imeneyi, pakali pano ndagula malo omwe ndikupanga ganizo loti ndimangepo kupatula apo golosale langali linadzadza tsopano ndipo ndikupeza phindu,” Katsika kulankhulapo.