Mkulu wa bungwe la National Economic Empowerment Fund Limited (NEEF) a Humphrey Mdyetseni anayendela ofesi za Kanengo, Lumbadzi, Dowa Boma, ndi Mponela ndi cholinga chofuna kuona momwe ntchito za bungweli zikuyendela makamaka katoleredwe komanso kagawidwe ka ndalama kwa a Malawi. Iwo afotokozela ogwira ntchito m’ma ofesi amenewa kuti atolere ndalama zonse zomwe zadutsa nyengo yobwezera ndalamazi ndi cholinga choti ena apindule nawo.

Ngongole ya NEEF imadalira kuti omwe anapindula nawo koyambilira akamabweza ena otsatira m’mbuyo akhale ndi mwai otenga nawonso. Izi zikuthandiza kuti a Malawi ochuluka apindule nawo kudzela mu ndalama imeneyi. Mkulu wa bungweli akhala akupitilizabe kuyendela ma ofesi a bungweli komaso anthu omwe apindula ndi ngongole ya NEEF, kuti amvetsetse momwe anthuwa anatengela ngongoleyi ndikugwiritsa ntchito ndalamayi potukula miyoyo yawo.

Anthu oposela 130,000 apindula ndingongole ya NEEF kuchokela February 2021 pomwe bungweli linayamba kugawa ngongole.

Leave a Comment