Azimayi a m’ma boma a Ntchisi komanso Dowa omwe ali m’magulu a bungwe lobwereketsa ngongole la National Economic Empowerement Fund Limited (NEEF) ndi okondwa pomwe alandira mphatso ya ma T-shirts kuchokera ku bungweli.
 
Azimayiwa anena izi la Mulungu masana pa mwambo omwe unachitikira m’boma la Dowa komanso Ntchisi pomwe bungwe la NEEF limakapereka ma Tshirts ku magulu omwe akuchita bwino pa kabwezedwe ka ngongole zawo.
NEEF yapanga izi ngati njira imodzi yothokozera magulu omwe akuchita bwino maka pakabwezedwe ka ngongole.
 
Bungweli lipitiriza kupereka mphatso kwa magulu komanso anthu omwe akuchita bwino m’maperekedwe awo komanso anatenga ngongole kachiwiri kapena kuposera apo ndipo zina mwa mphatsozi ndi monga ma T-shirts.
Amai kuvina ku Ntchisi alandira mphatso ya T-shirt ya NEEF
Ndipo m’modzi wa m’khalapampando wagulu la Chimwemwe women, Loveness Isaac kuchokera kwa mfumu yayikulu Chakhadza wati iwo ndiwosangalala kwambiri powona kuti Bungweli lawaganizira ndi mphatso ya ma T-shirts ndipo anenetsa kuti iwo apitiriza kubweza ngongole pozindikira kuti anthu ena apindule nawonso.
 
“Izi ndi zinthu zosowa kwambiri chifukwa ife takhala tikutenga ngongole ku mabungwe osiyanasiyana koma mabungwe enawa sadatipatseko mphatso ngati iyi ndipo tinene pano kuti mphatso iyi itipatsa mangolomera akabwezedwe kabwino ndicholingachakuti titengenso ngongole ina,” Isaac kufotokoza.
 
Popitiriza kufotokoza Mayiwa anenetsa kuti Ngongole ya NEEF ndi yabwino chifukwa chakuti chiwongola dzanja chake ndichochepa ndipo siyovuta kubweza.
Ogwira ntchito ku NEEF kupereka ma t-shirt
Pothirira ndemanga wapampando wa gulu la Chinkhonje Women Rose Levison kuchokera kwa fumu yayikulu Nthondo wati ngati magulu omwe amapanganso za Banki M’khonde akulimbikitsika ndi ngongole ya bungweli ndipo iwo apitiriza kubweza monga mwamalonjezano ndi bungweli.
 
“Ife ndife anthu achimwemwe ndikubwera kwanu potipatsa mphatso imeneyi ndipo izi zipangitsa magulu enanso kuti azibweza mwamachawi kuti nawonso adzapatsidwe mphatso imeneyi,”Levison kufotokoza.
 
Iye wapempha bungweli kuti lisasiyire pomwepa koma liwaganizirenso ndi Msalu kuti magulu awo azidziwika mosavuta ndi magulu omwe amatenga ngongole ku ma bungwe ena.
 
Bungweli lapereka ma T-shirts osachepera makumi asanu ndi ndi imodzi (60) kumagulu asanu ndi imodzi kuchokera m’ma boma a Ntchisi komanso Dowa. Maguluwa ndi monga Chinkhonje Women, Tipindula Women, ndi Tikondane women kuchokera m’boma la Ntchisi Komanso Changu women,Chimwemwe women ndi gulu la Mbunge women kuchokera m’boma la Dowa.

Leave a Comment