Bungwe la NEEF lachita mkumano ndi adindo am’boma la Mangochi umene ukuchitikira pa Hall ya Khonsolo ya Bomali.

Cholinga cham’kumanowu malinga ndi mkulu wa Bungwe la NEEF a Humphrey Mdyetseni, ndikufuna kufotokozera adindowa momwe NEEF ikugwilira ntchito m’bomali komanso kuwapempha kuti athandize bungweli kuti lizikwanitsa kutolera ngongole zonse zomwe lapereka m’boma la Mangochi.

Malinga ndi a Mdyetseni, NEEF yagawa ndalama zokwana K1.52 Billion kwa anthu oposa 3,742 mboma la Mangochi lokha ndipo padakali pano bomali liri pa 87.2% pakubweza ndalamazi.

Iwo anayamikira madera a Makanjira ndi Malombe amene akubweza bwino ngongolezi ngakhale kuti kumaderawa kulibe ma bank ndipo anthu amayenda ulendo wautali kupita ku Mangochi Boma kukabweza ndalamazi ku Bank.

Mwamadera amene sakubweza bwino ngongolezi malinga ndi a Mdyetseni ndi Mangochi South komanso Mangochi West.

Padakali pano bungwe la NEEF lagawa ndalama zokwana K36 Billion kwa anthu oposa 105, 000 m’maboma onse 28 m’dziko muno ndipo ndalama zimene zimene zabwezedwa ndi 63%.

Ichi ndi chifukwa chake NEEF ikuchita mikumano ndi adindo m’maboma onse kuti awadziwitse zakufunika kuti anthu am’madera awo aziweza ngongolezi pofuna kuti thumbali lipindulire anthu ambiri m’dziko muno.

A Lilian Patel ndi aphungu ena anali a m'boma la Mangochi anali nao ku mkumanowu

Mwa adindo amene anali kumkumanowu ndi aphungu ambomali monga phungu wa Mangochi South a Lilian Patel amene alinso mtsogoleri wachipani cha United Democrat Front (UDF); Phungu waku Mangochi West a Reuben Kanyama; Phungu wa Mangochi Central a Victoria Kingstone; ndi Phungu waku Mangochi Moneybay a Ralph Juma.

Kumkumanowu kunalinso mafumu am’bomali, Makhansala, mamembala a ADCs ndi ma VDC.

Leave a Comment