MAGULU AMENE AKULANDIRA NGONGOLE

Bungwe la National Economic Empowerment Fund Limited (NEEF) likufuna kuzidziwitsa a Malawi kuti lanayamba kupereka ngongole m’sabata yoyamba ya mwezi wa February 2021. Ili ndi gawo loyamba lopereka ngongole m’chaka chino cha 2020/ 2021. Ndipo ndondomeko yonse ili motere:

Gawo Loyamba: Ngongole za Magulu

M’gawo ili NEEF ikupereka ngongole kwa magulu amene ali ndi mtima wopanga bizinesi. Pofika sabata yachitatu ya February, magulu okwana 907 ndi amene ali mkaundula wa NEEF ndipo ayamba kulandira ngongole zawo. Pamaguluwa, 634 ndi magulu amai, 238 ndi magulu achinyamata ndipo 35 ndi magulu ophatikiza abambo ndi amai. NEEF igwiritsa ntchito ndalama zokwana K1.5 billion kumaguluwa.

Ogwira ntchito ku NEEF pamodzi ndi magulu akudera la Makawa m'boma la Mangochi.

Padakali pano, ntchito yolemba magulu ikupitilirabe m’maboma onse. Kwa onse amene anatenga nao ngongole za MEDF ndipo sanabweze sakuloledwa  kutenga nao ngongole zapanozi kufikira abweze ngongole zoyambazo.

Gawo Lachiwiri: Ngongole za Munthu Payekha

Ntchito yolemba anthu kuti atenge nao ngongole zimene NEEF izipereka kwa munthu payekha iyamba sabata yoyamba ya mwezi wa March ndipo iziyendera limodzi ndi ntchito yolemba magulu imene tayamba kale. Onse amene ali ndi chidwi chofuna kuyamba kapena kukuza bizinesi zawo akuyenera kupita ku maofesi a NEEF akudera lawo kuti akauzidwe ndondomeko zimene angatsate kuti apindule ndi ngongolezi. Mitundu yangongole imene tizipereka m’gawoli ili motere:

  • Business Loans: Ngongoleyi akhoza kutenga ndi munthu payekha kapena magulu amene ali ndi bizinesi zing’ono-zing’ono komanso bizinesi zokulirapo
  • Agricultural Loans: Ngongoleyi akhoza kutenga munthu payekha kapenanso gulu kuti apeze zipangizo zakumunda monga mbewu, fetileza ndi zina
  • Trade Finance Loans: Ngongole imene akhoza kutenga munthu payekha ngati wapeza maoda kapena ntchito ina yoti agwire ndipo alibe ndalama zogwilira ntchitoyi
  • Payroll Loans: Iyi ndi ngongole imene munthu wolembedwa ntchito m’boma kapena thambi zaboma komanso ogwira ntchito kumakampani amene siaboma akhoza kutenga.

Onse amene akufuna kutenga nao ngongolezi akuyenera kupita ku maofesi a NEEF amene ali nao pafupi kuti akauzidwe ndondomeko zotengera ngongolezi kapena mukhoza kuimba foni kwa akulu-akulu a NEEF a m’zigawo amene nambala zawo taika m’musimu

NEEF Ilibe Amkhala Pakati

Bungwe la NEEF likufunanso kutsindika kuti silinapeze anthu kapena magulu a anthu kuti azigwira ntchito m’amalo mwake. Ntchitoyi ikumagwiridwa ndi ogwira ntchito ku NEEF okha ndipo NEEF ikadzafuna kupeza anthu oti athandizire ntchitoyi dziko la Malawi lizadziwitsidwa. Choncho anthu akuyenera kusamala za akapsali ena amene akumanamiza anthu ndikumawatengera ndalama. Dziwani kuti bungwe la NEEF silizatengapo mbali ngati mukanike kutsatira ndondomeko zoyenera.

Mkulu wa NEEF Humphrey Mdyetseni akuwunika magulu achinyamata pa boma la Dowa

Ntchito Yotolera Ngongole za MEDF

Ntchito yotolera ngongole zonse zimene zinaperekedwa ndi bungwe lakale lija la MEDF ili mkati. Padakali pano tikukonza maina onse a anthu amene anatenga ngongolezi ndipo tatsala pang’ono kutsiriza ntchitoyi. Posachedwapa tiyamba kuyendera anthu onse kuti ayambe kubweza ngongolezi ku Boma. Ndizofunika kuti onse amene anatenga ngongolezi abweze kuti tipereke kwa anthu ena amene akusowa mpamba kuti nawo apeze mwai woyamba bizinesi.

Bungwe la NEEF likufuna lipezerepo mwayi ndi kuthokoza kwambiri anthu onse amene anayamba kale kubweza ngongolezi paokha kuti apitirize kutero ndipo akamaliza akhala ndi mwayi wotenga ngongole ina mwinanso yokulirapo. Kwa iwo amene sanayambe kubweza tikuwalimbikitsa kuti ayambe pano kuopa kuti ngongole yawo izikula chifukwa cha chindaputsa chimene chidzionjezeredwa pamwamba ngati azipitiriza kuzemba kubweza ngongole za MEDF.

Ntchito yolemba anthu kuti apindule ndi ngongole za NEEF yakhuzidwa ndi mliri wa Covid-19. Ntchito yokumana ndi magulu kuti awunikidwe ndi kuwapatsa ngongolezi yapangitsa kuti ogwira ntchito ena ku NEEF adwale matenda a Covid-19 ndipo ena adzipatula kukakhala kwa okha monga mwa malamulo achipatala. Ndipo izi zatibwezeretsa m’mbuyo. Pofunanso kuonesetsa kuti malo ogwilira ntchito muli anthu ochepa, ogwira ntchito ena ku NEEF akugwirira kunyumba malinga ndi ndondomeko zimene boma lakhazikitsa ndipo ichi ndi chifukwa chake madera ena sitinawafikire.

Ogwira ntchito ku NEEF akuphunzitsa magulu paboma la Rumphi.

Akulu-akulu Am’zigawo Amene Mukhoza Kuwaimbira Foni

M’chigawo Chakumwera: Mr. Thomas Nthenda 0881 906 696 ndipo ma ofesi a NEEF m’chigawochi ali kumadera awa: Blantyre Branch m’nyumba yakale ya Press Properties ku Namiwawa moyang’anizana ndi Multi Choice Malawi; Chikwawa Branch moyang’anizana ndi polisi ya Chikwawa pafupi ndi Banki ya FDH; Luchenza Branch m’nyumba ya Upstair Lodge; ndipo Phalombe Branch ili pa Boma moyang’anizana ndi ma ofesi a DHO.

M’chigawo Chapakati: Mr. Wilson Namwera 0881 820 992/ 01 754 124 ndipo ma ofesi a NEEF ali motere m’chigawochi: Lilongwe Branch kuseli kwa Bridge View Hotel; Mchinji Branch pafupi ndi PVHO; Mponela Branch m’nyumba ya Super Sink; Kasungu Branch pafupi ndi Kasungu Community Hall; Salima Branch m’nyumba ya Visco City mumseu wopita ku Sengabay; ndipo Nkhotakota Branch ili m’nyumba ya Yanu-Yanu mumseu wopita ku polisi ya Nkhotakota.

M’chigawo Chakum’mawa: Mrs. Esmie Chisepeya Jambo 0882 426 670 ndipo ma ofesi a NEEF ali motere m’chigawochi: Zomba Branch m’nyumba ya FDH Banki; Liwonde Branch pafupi ndi National Banki; Mangochi Branch kumaofesi akale a Water; ndipo Ntcheu Branch ili moyang’anizana ndi Small Holder Fertilizer Revolving Fund.

M’chigawo Chakumpoto: Mr. Felix Tembo 01 311 567, 01 312 501, 0888 877 400 ndipo ma ofesi a NEEF ali motere m’chigawochi: Mzimba Branch ili kuma ofesi a DC; Mzuzu Branch ili m’nyumba yakale ya OIBM pafupi ndi Kips Restaurant; Rumphi Branch ili m’maofesi a DC; Nkhatabay Branch ili m’nyumba ya Fisheries; Karonga Branch ili pafupi ndi transmita ya MBC; ndipo Chitipa Branch ili m’maofesi a DC.

Mukafuna kumva zambiri imbani foni ku likulu la NEEF pa 09999 41 333/ 09999 38 333 kapena tumizani kalata yanu ku info@neef.mw/ complaints@neef.mw.

MAGULU AMENE AKULANDIRA NGONGOLE

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

Scroll to top